Intro:
apa ndiye ndagwa ndagwa/i think ndingolemba kalata ku church chifukwa apa nde ofunika chithandizo bax andipemphelele/eeh ndiauze mavuto amene ndaona ine/aah yeah ambuye mundithandize ndasochela
mmm ok yeah
choyamba ndati ndipeleke moni/kwa ma BA anzanga mulibwanji/ ine ndilibwino kunkhani yaphysical koma spiritual sizilibho/pamaso panu ndimaoneka ngati munthu wangwiro/koma mumtima mwanga mwangodzadza ndiuchimo mkwiyo kuphatikizanso umbombo/ndikaunika mmoyo mwanga palibe chabwino/inde mumati ine ndinabona koma ndikukaika/chifukwa moyo wanga sukusintha/chikondi ndilibe/kukhululuka ndikukanika/chonde mundipemphelele/anzanga ndaona chichristu nchovuta/ndaonanso kuti pandekha sindikwanitsa/ndichifukwa kalatayi ndikulemba/mundithandize ndasowa mtengo wogwira/anzanga ine kuno zandivuta/
Dieser text wurde 340 mal gelesen.